29 Iwo adzakuchitira zinthu zosonyeza kuti amadana nawe ndipo adzatenga zinthu zonse zimene unazipeza movutikira+ nʼkukusiya wosavala ndi wamaliseche. Umaliseche umene unauonetsa pochita chiwerewere, khalidwe lako lonyansa ndiponso uhule wako zidzaonekera poyera.+