7 ine nditambasula dzanja langa nʼkukulangani ndipo ndikuperekani kwa anthu a mitundu ina kuti akutengeni. Ndidzakuwonongani kuti musakhalenso mtundu wa anthu ndipo ndidzakuchotsani pakati pa mayiko ena.+ Ndidzakufafanizani ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’