-
Ezekieli 32:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Iwo amupangira bedi pakati pa anthu amene aphedwa limodzi ndi gulu la anthu ake onse amene ankamutsatira, onse azungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osadulidwa, amene aphedwa ndi lupanga chifukwa anachititsa kuti anthu amene akukhala mʼdziko la anthu amoyo azikhala mwamantha. Iwo adzachita manyazi limodzi ndi anthu amene akutsikira kudzenje.* Iye waikidwa mʼmanda pakati pa anthu ophedwa.
-