27 Kodi amenewa sadzagona limodzi ndi asilikali amphamvu osadulidwa amene anaphedwa, amene anatsikira ku Manda limodzi ndi zida zawo zankhondo? Iwo adzaika malupanga awo pansi pa mitu yawo ndipo machimo awo adzawaika pamafupa awo chifukwa asilikali amphamvuwo anawononga dziko la anthu amoyo.