-
Ezekieli 33:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Iwe mwana wa munthu, uza anthu a mtundu wako kuti, ‘Munthu wolungama akapanduka, zinthu zolungama zimene ankachita, sizidzamupulumutsa.+ Munthu woipa akasiya zoipa zakezo, zoipazo sizidzachititsa kuti apunthwe.+ Komanso pa tsiku limene munthu wolungama wachimwa, zinthu zolungama zimene ankachita zija sizidzamuthandiza kuti apitirize kukhala ndi moyo.+
-