2 “Iwe mwana wa munthu, losera zoipa zimene zidzachitikire abusa a Isiraeli. Losera ndipo uuze abusawo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka abusa a Isiraeli,+ amene akhala akungodzidyetsa okha! Kodi abusa ntchito yawo si kudyetsa nkhosa?+