14 Nkhosazo ndidzazidyetsera mʼmalo a msipu wabwino ndipo malo amene zizidzadya msipu adzakhala kumapiri ataliatali a ku Isiraeli.+ Kumeneko zizidzagona pansi mʼmalo abwino kwambiri odyetserako ziweto+ ndipo zizidzadya msipu wabwino kwambiri mʼmapiri a ku Isiraeli.