23 Iwo sadzadziipitsanso ndi mafano awo onyansa, zochita zawo zonyansa ndi zolakwa zawo zonse.+ Ndidzawapulumutsa ku zochita zawo zosakhulupirika zimene zinachititsa kuti achimwe ndipo ndidzawayeretsa. Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+