16 Mofanana ndi mitambo imene yaphimba dziko, iwe udzabwera kudzaukira anthu anga Aisiraeli. Mʼmasiku otsiriza, ine ndidzakubweretsa kuti uukire dziko langa+ nʼcholinga choti anthu a mitundu ina adzandidziwe ndikamadzadziyeretsa pamaso pawo, kudzera mwa iwe Gogi.”’+