20 Chifukwa cha ine, nsomba zamʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zilombo zakutchire, nyama zonse zimene zimakwawa panthaka ndiponso anthu onse apadziko lapansi, zidzanjenjemera. Mapiri adzagwa,+ malo otsetsereka adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwera pansi.’