9 Anthu amene akukhala mʼmizinda ya Isiraeli adzapita kukakoleza moto pogwiritsa ntchito zida zankhondo. Zida zake ndi zishango zazingʼono ndi zishango zazikulu, mauta ndi mivi, zibonga ndi mikondo ingʼonoingʼono. Iwo adzagwiritsa ntchito zida zimenezi kwa zaka 7 pokoleza moto.+