3 Zimene ndinaonazo zinali zofanana ndi zimene ndinaona mʼmasomphenya ena pamene ndinapita kukawononga mzinda. Ndinaona zinthu zofanana ndi zimene ndinaona mʼmphepete mwa mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi.