5 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, uchite chidwi, uonetsetse ndipo umvetsere mwatcheru zonse zimene ndikuuze zokhudza malangizo ndi malamulo a kachisi wa Yehova. Uonetsetse khomo lolowera mʼkachisi ndi makomo onse otulukira mʼmalo opatulika.+