4 Malo amenewa adzakhale gawo lopatulika la ansembe mʼdzikoli,+ omwe ndi atumiki apamalo opatulika, amene amayandikira kwa Yehova nʼkumamutumikira.+ Malo amenewa adzakhala oti adzamangepo nyumba zawo komanso adzakhala malo opatulika omangapo kachisi.