9 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatopa nanu inu atsogoleri a Isiraeli!
Siyani ziwawa ndi kupondereza anthu anga ndipo muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Lekani kulanda zinthu za anthu anga,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.