11 Muyezo wa efa komanso wa mtsuko woyezera uzikhala wosasinthasintha. Muyezo wa mtsuko uzikhala wokwana gawo limodzi la magawo 10 a homeri ndipo muyezo wa efa uzikhala wokwana gawo limodzi la magawo 10 a homeri. Muyezo wa homeri ukhale muyezo wa nthawi zonse.