15 Pa ziweto zonse mu Isiraeli, muzipereka nkhosa imodzi kuchokera pa nkhosa 200 zilizonse. Muzidzagwiritsa ntchito zinthu zonsezi popereka nsembe zambewu,+ nsembe zopsereza zathunthu+ ndi nsembe zamgwirizano+ pofuna kuphimba machimo a anthu,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.