-
Ezekieli 45:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Kwa masiku 7 a chikondwererocho, iye azipereka kwa ansembe nyama zoti ziperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopsereza yathunthu. Azipereka ngʼombe 7 zazingʼono zamphongo ndi nkhosa 7 zamphongo. Nyama zimenezi zizikhala zopanda chilema ndipo azizipereka tsiku lililonse kwa masiku 7 amenewo.+ Aziperekanso mbuzi yamphongo tsiku lililonse kuti ikhale nsembe yamachimo.
-