10 Gawo limeneli likhale chopereka chopatulika cha ansembe.+ Mbali yakumpoto, gawoli likhale mikono 25,000. Mbali yakumadzulo likhale mikono 10,000. Mbali yakumʼmawa likhale mikono 10,000 ndipo mbali yakumʼmwera likhale mikono 25,000. Malo opatulika a Yehova adzakhala pakati pa gawo limeneli.