-
Ezekieli 48:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Malo amene atsala kumbali zonse za chopereka chopatulika ndiponso ya malo a mzinda akhale a mtsogoleri wa anthu.+ Malowa adzachita malire ndi malo omwe ndi chopereka, amene akukwana mikono 25,000 kumʼmawa ndi kumadzulo. Malowo achite malire ndi malo amene anaperekedwa aja ndipo akhale a mtsogoleri wa anthu. Malo omwe ndi chopereka chopatulika komanso malo opatulika a kachisi aja akhale pakati pa malo a mtsogoleriwa.
-