2 Kenako Yehova anapereka Mfumu Yehoyakimu ya Yuda mʼmanja mwake,+ limodzi ndi zina mwa ziwiya za mʼnyumba ya Mulungu woona. Nebukadinezara anatenga ziwiyazo nʼkupita nazo kudziko la Sinara,+ kunyumba ya mulungu wake ndipo anakaziika mʼnyumba yosungiramo chuma ya mulungu wake.+