4 Inalamula kuti abweretse achinyamata amene analibe chilema chilichonse, ooneka bwino, anzeru, odziwa zinthu, ozindikira+ komanso amene akanatha kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Iye ankayenera kuwaphunzitsa chilankhulo komanso zinthu zina zimene Akasidi analemba.