26 Nebukadinezara anayandikira khomo la ngʼanjo yoyaka motoyo nʼkunena kuti: “Shadireki, Misheki ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wamʼmwambamwamba,+ tulukani ndipo mubwere kuno!” Atatero, Shadireki, Misheki ndi Abedinego anatuluka pakati pa motowo.