-
Danieli 4:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Pa nthawi imeneyo Danieli, amene dzina lake ndi Belitesazara,+ anada nkhawa kwa kanthawi ndipo anachita mantha.
Mfumuyo inamuuza kuti, ‘Iwe Belitesazara, usachite mantha ndi malotowa komanso kumasulira kwake.’
Belitesazara anayankha kuti, ‘Inu mbuyanga, zikanakhala bwino malotowa akanakhala okhudza anthu amene amadana nanu. Zikanakhalanso bwino kumasulira kwake kukanakhala kokhudza adani anu.
-