-
Danieli 5:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Mu ufumu wanu muli munthu amene ali ndi mzimu wa milungu yoyera. Mʼmasiku a bambo anu, anthu anazindikira kuti munthuyu ndi wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndiponso ali ndi nzeru zofanana ndi nzeru za milungu.+ Ndiyeno bambo anu, Mfumu Nebukadinezara, anamuika kuti akhale mkulu wa ansembe ochita zamatsenga, anthu okhulupirira mizimu, Akasidi* ndi anthu okhulupirira nyenyezi.+ Ndithudi mfumu, bambo anu anamupatsa udindo umenewu.
-