-
Danieli 5:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo mtima wake unasinthidwa nʼkukhala ngati wa nyama moti anayamba kukhala limodzi ndi abulu akutchire. Iye ankadya udzu ngati ngʼombe ndipo thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anadziwa kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa munthu aliyense amene akufuna kumupatsa.+
-