-
Danieli 5:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Mʼmalomwake mwadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba+ ndipo munalamula anthu kuti akubweretsereni ziwiya zamʼnyumba yake.+ Ndiyeno inuyo, nduna zanu, adzakazi anu ndi akazi anu ena mwamwera vinyo mʼziwiya zimenezi ndipo mwatamanda milungu yasiliva, yagolide, yakopa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala imene siona, kumva kapena kudziwa chilichonse.+ Koma Mulungu amene amakupatsani mpweya komanso amene ali ndi mphamvu zolamulira moyo wanu, simunamulemekeze.+
-