-
Danieli 6:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Pa nthawiyo, nduna zapamwamba ndi masatarapi aja ankafufuza zifukwa zoti amuimbire mlandu Danieli pa nkhani zokhudza mmene ankayendetsera zinthu mu ufumuwo. Koma iwo sanapeze chifukwa chilichonse chomuimbira mlandu kapena chinthu chilichonse chachinyengo chimene anachita. Zinali choncho chifukwa Danieli anali wokhulupirika ndipo iwo anapeza kuti sankanyalanyaza udindo wake kapena kuchita zachinyengo zilizonse.
-