25 Mochenjera idzachita zinthu mwachinyengo kuti zinthu ziiyendere bwino ndipo idzadzitukumula kwambiri mumtima mwake. Pa nthawi yamtendere idzawononga anthu ambiri. Mfumuyo idzalimbana ngakhale ndi Kalonga wa akalonga, koma idzathyoledwa osati ndi dzanja la munthu.