12 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Iwe Danieli, usachite mantha.+ Mawu ako akhala akumveka kuyambira tsiku loyamba pamene unatsegula mtima wako kuti umvetse tanthauzo la zinthu zimenezi, ndiponso pamene unadzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, ndipo ine ndabwera chifukwa cha mawu akowo.+