4 Koma mfumuyo ikadzayamba kulamulira, ufumu wake udzasweka ndipo udzagawanika nʼkutengedwa ndi mphepo 4 zakumwamba,+ koma sudzapita kwa mbadwa zake ndipo maufumuwo sadzafanana ndi ufumu wake. Zimenezi zidzachitika chifukwa ufumu wake udzazulidwa nʼkuperekedwa kwa ena.