36 Mfumuyo idzachita zofuna zake ndipo idzadzikweza ndi kudzikuza kuposa mulungu aliyense. Iyo idzalankhula zinthu zodabwitsa zotsutsana ndi Mulungu wa milungu.+ Mfumuyo idzapambana mpaka nthawi ya mkwiyo itatha, chifukwa zimene Mulungu wakonza ziyenera kuchitika.