18 Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zilombo zakutchire mʼmalo mwa anthu anga,+
Komanso ndi mbalame zouluka mumlengalenga ndi zinthu zokwawa panthaka.+
Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo mʼdzikolo.+
Ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere.+