3 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Pita ukayambenso kukonda mkazi amene akukondedwa ndi mwamuna wina ndipo akuchita chigololo.+ Ukamukonde ngati mmene Yehova amakondera Aisiraeli,+ ngakhale kuti iwo amalambira milungu ina+ komanso amakonda makeke a mphesa.”