-
Hoseya 4:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Iwo amapereka nsembe pamwamba pa mapiri akuluakulu,+
Ndipo amapereka nsembe zautsi pamapiri angʼonoangʼono.
Amachitanso zimenezi pansi pa mitengo yokhala ndi nthambi zambiri ndi masamba ambiri, pansi pa mitengo ya mlanje ndiponso pa mtengo uliwonse waukulu,+
Chifukwa mitengo imeneyi imakhala ndi mthunzi wabwino.
Nʼchifukwa chake ana anu aakazi amachita uhule
Ndipo akazi a ana anu amachita chigololo.
-