10 “Isiraeli ndinamupeza ali ngati mphesa zamʼchipululu.+
Ndinaona makolo anu ali ngati nkhuyu zoyambirira pamtengo wa mkuyu.
Koma anapita kwa Baala wa ku Peori,+
Anadzipereka kwa chinthu chochititsa manyazichi.+
Ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene ankachikondacho.