5 Oyendetsa chombo anachita mantha kwambiri ndipo aliyense anayamba kuitana mulungu wake kuti amuthandize. Iwo anayamba kuponya mʼnyanja katundu amene anali mʼchombocho kuti chipepukidwe.+ Apa nʼkuti Yona atatsikira mkatikati mwa chombocho nʼkugona tulo tofa nato.