5 Zonsezi zidzachitika chifukwa chakuti Yakobo wandigalukira.
Ndiponso chifukwa cha machimo a nyumba ya Isiraeli.+
Kodi wachititsa kuti Yakobo andigalukire ndani?
Kodi si anthu a ku Samariya?+
Wachititsa ndani kuti Yuda akhale ndi malo okwezeka?+
Si anthu a ku Yerusalemu kodi?