4 Pa tsikulo anthu adzanena mwambi wokhudza anthu inu.
Ndipo adzaimba nyimbo yokulirirani.+
Adzanena kuti: “Ife ndiye tatha basi!+
Wachititsa kuti cholowa cha anthu amtundu wathu chiperekedwe kwa anthu ena. Talandidwa cholowa chathu.+
Iye wapereka minda yathu kwa anthu osakhulupirika.”