12 Ndiyeno Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli,+ Yoswa mwana wa Yehozadaki+ mkulu wa ansembe ndiponso anthu ena onse anamvera mawu a Yehova Mulungu wawo ndi a mneneri Hagai, chifukwa Yehova Mulungu wawo ndi amene anamutuma. Ndipo anthuwo anayamba kuchita mantha chifukwa cha Yehova.