4 ‘Koma tsopano limba mtima iwe Zerubabele. Limba mtima iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe,’ watero Yehova.
‘Limbani mtima anthu nonse amʼdzikoli+ ndipo gwirani ntchito,’ watero Yehova.
‘Pakuti ine ndili ndi inu,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.