-
Zekariya 1:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ndiyeno ndinafunsa kuti: “Kodi awa abwera kudzatani?”
Mngeloyo anayankha kuti: “Zimenezi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda moti panalibe amene anatha kudzutsa mutu wake. Amisiriwa adzabwera kudzaopseza nyangazi ndipo adzawononga nyanga za mitundu ina ya anthu amene anakweza nyanga* zawo poukira dziko la Yuda kuti abalalitse anthu ake.”
-