7 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ukayenda mʼnjira zanga ndi kutsatira malamulo anga, udzakhala woweruza wa anthu a mʼnyumba yanga+ ndipo uzidzasamalira mabwalo a nyumba yanga. Komanso ndidzakulola kumafika pamaso panga ngati mmene amachitira aima apawa.’