6 Pa tsiku limenelo, ndidzachititsa mafumu a Yuda kukhala ngati mbaula zamoto pakati pa mitengo komanso ngati miyuni yamoto pamilu ya tirigu.+ Iwo adzatentha anthu a mitundu yonse yowazungulira, kumanja ndi kumanzere.+ Ndipo anthu a ku Yerusalemu adzakhalanso pamalo awo mumzinda wa Yerusalemu.+