12 Anthu amʼdziko lonselo adzalira mokuwa. Banja lililonse lizidzalira palokha. Banja la nyumba ya Davide lizidzalira palokha ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. Banja la nyumba ya Natani+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha.