13 “Pali chinthu chinanso chimene anthu inu mukuchita ndipo chikuchititsa kuti guwa lansembe la Yehova lidzaze ndi misozi, kulira ndi kubuula. Chifukwa cha zimenezi, nsembe zanu zimene mumapereka ngati mphatso nʼzosavomerezeka kwa iye ndipo sakusangalala ndi chilichonse chochokera mʼmanja mwanu.+