22 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima+ mʼbale wake wapalamula mlandu wa kukhoti. Ndipo aliyense wonenera mʼbale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Komanso aliyense wonena mnzake kuti, ‘Ndiwe chitsiru!’ adzapita ku Gehena wamoto.+