64 Choncho lamulani kuti akhwimitse chitetezo pamandapo mpaka tsiku lachitatu, kuti ophunzira ake asabwere kudzamuba+ nʼkumauza anthu kuti, ‘Anaukitsidwa kwa akufa!’ Chifukwa chinyengo chotsirizachi chidzakhala choipa kwambiri kuposa choyamba chija.”