21 Yesu anamuyangʼana ndipo anamukonda. Kenako anamuuza kuti, “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita ukagulitse zinthu zimene uli nazo ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+