14 Atafika, iwo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo simuchita zinthu pongofuna kusangalatsa munthu, chifukwa simuyangʼana maonekedwe a anthu, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. Kodi nʼzololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?